17. Mfumuyi inaziyenga pa cidikha ca ku Yordano, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda.
18. Ndipo Solomo anazipanga zipangizo izi zonse zocurukadi, pakuti kulemera kwace kwa mkuwa sikunayeseka.
19. Solomo anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolidi lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;
20. ndi zoikapo nyali ndi nyali zace za golidi woona, zakuunikira monga mwa cilangizo cace cakuno ca moneneramo;