1. Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwace mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono khumi.
2. Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wace mikono isanu; ndi cingweca mikono makumi atatu cinalizunguniza.
3. Ndi pansi pace panali mafanziro a ng'ombe zakulizinga khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pace. Ng'ombezo zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.