16. Ndi Safani anamuka nalo buku kwa mfumu, nabwezeranso mau kwa mfumu, ndi kuti, Zonse mudazipereka kwa anyamata anu alikuzicita.
17. Nakhuthula ndarama zinapezeka m'nyumba ya Yehova, nazipereka m'manja a akapitao ndi m'manja a anchito.
18. Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.
19. Ndipo kunali, atamva mfumu mau a cilamulo, anang'amba zobvala zace.
20. Mfumu niuza Hilikiya, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Abidoni mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,
21. Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala m'Israyeli ndi Yuda, za mau a m'buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukuru; popeza makolo athu sanasunga mau a Yehova kucita monga mwa zonse zolembedwa m'bukumu.