1. Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu cimodzi.
2. Nacita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira za Davide kholo lace, osapambuka ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.
3. Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lace; ndipo atakhala zaka khumi ndi cimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzicotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga,