2 Mbiri 30:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israyeli lonse, kuyambira Beereseba kufikira ku Dani, kuti abwere kucitira Yehova Mulungu wa Israyeli Paskha ku Yerusalemu; pakuti nthawi yaikuru sanacita monga mudalembedwa.

6. Tsono amtokoma anamuka ndi akalata ofuma kwa mfumu ndi akuru ace mwa Israyeli ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israyeli, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isake, ndi Israyeli, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m'dzanja la mafumu a Asuri.

7. Ndipo musamakhala ngati makolo anu ndi abale anu, amene anai akwira Yehova Mulungu wa makolo ao, motero kuti anawapereka apasuke, monga mupenya,

8. Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ace opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wace waukali utembenuke kwa inu.

9. Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza cifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa cisomo ndi cifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye,

10. Ndipo amtokoma anapitira m'midzi m'midzi mwa dziko la Efraimu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola.

11. Komatu ena a Aseri ndi Manase ndi a Zebuloni anadzicepetsa, nadza ku Yerusalemu.

12. Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kucita cowauza mfumu ndi akuru mwa mau a Yehova.

13. Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kucita madyerero a mkate wopanda cotupitsa mwezi waciwiri, msonkhano waukuru ndithu.

2 Mbiri 30