24. Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kucipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo iri ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.
25. Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ace kutenga zofunkha zao, anapezako cuma cambiri, ndi mitembo yambiri, ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinacuruka.
26. Ndi tsiku lacinai anasonkhana m'cigwa ca Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo, Cigwa ca Beraka, mpaka lero lino.
27. Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kumka ku Yerusalemu ndi cimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao.