2 Mbiri 2:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Solomo anatumiza kwa Huramu mfumu ya Turo, ndi kuti, Monga momwe munacitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundicitire ine momwemo.

4. Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pace zonunkhira za pfungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wacikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa madyerero oikika a Yehova Mulungu wathu. Ndiwo macitidwe osatha m'Israyeli.

5. Ndipo nyumba nditi ndimangeyi ndi yaikuru; pakuti Mulungu wathu ndiye wamkuru woposa milungu yonse.

6. Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira cofukiza ndiko?

7. Ndipo tsono munditumizire munthu wa luso lakucita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota ziri zonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine m'Yuda ndi m'Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.

2 Mbiri 2