16. ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebano monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.
17. Ndipo Solomo anawerenga alendo Onse okhala m'dziko la Israyeli, monga mwa mawerengedwe aja atate wace Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.
18. Ndipo anaika zikwi makumi asanu ndi awiri za iwowa asenze mirimo, ndi zikwi makumi asanu ndi atatu ateme m'mapiri, ndi akapitao zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndilimodzi agwiritse anthu nchito.