2 Mbiri 18:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehosafati tsono anali nacocuma ndi ulemu zomcurukira, nacita cibale ndi Ahabu.

2. Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zocuruka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Gileadi.

3. Nati Ahabu mfumu ya Israyeli kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Gileadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.

4. Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israyeli, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.

5. Pamenepo mfumu ya Israyeli anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Gileadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.

2 Mbiri 18