2 Mafumu 7:18-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo kunacitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa cipata ca Samariya;

19. ndipo kazembe uja adayankha munthu wa Mulunguyo, nati, Taonani tsono, Yehova angacite mazenera m'mwamba, cikacitika ici kodi? Nati iye, Taona, udzaciona ici ndi maso ako, koma osadyako ai;

20. kudamcitikira momwemo; popeza anthu anampondereza pacipata nafa iye.

2 Mafumu 7