2 Mafumu 4:19-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Natikwa atate wace, Mutu wanga, mutu wanga! Pamenepo anati kwa mnyamata, Umnyamule umuke naye kwa amace.

20. Namnyamula, napita naye kwa amace. Ndipo anakhala pa maondo ace kufikira usana, namwalira.

21. Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, naturuka, namtsekera.

22. Naitana mwamuna wace, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi buru mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.

2 Mafumu 4