2 Mafumu 19:29-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndi ici ndi cizindikilo cako: caka cino mudzadya za mphulumukwa, ndi caka ca mawa za mankhokwe, ndi caka camkuca muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zace.

30. Ndipo opulumuka a nyumba ya Yuda otsalawo adzaphukanso mizu, ndi kupatsa zipatso pamwamba.

31. Pakuti ku Yerusalemu kudzaturuka otsala, ndi akupulumukawo ku phiri la Ziyoni; cangu ca Yehova cidzacita ici.

2 Mafumu 19