24. Ndipo mfumu ya Asuri anabwera nao anthu ocokera ku Babulo, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Safaravaimu, nawakhalitsa m'midzi ya Samariya, m'malo mwa ana a Israyeli; nakhala iwo eni ace a Samariya, nakhala m'midzi mwace.
25. Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaopa Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa.
26. Motero ananena ndi mfumu ya Asuri, kuti, Amitundu aja mudawacotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m'midzi ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; cifukwa cace anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, irikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.
27. Pamenepo mfumu ya Asuri analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawacotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.
28. Nadza wina wa ansembewo adawacotsa ku Samariya, nakhala ku Beteli, nawalangiza m'mene azimuopera Yehova.