19. Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ace onse, asasowe mmodzi; pakuti ndiri nayo nsembe yaikuru yocitira Baala; ali yense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Kama Yehu anacicita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.
20. Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.
21. Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisrayeti onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala pha.
22. Nati kwa iye wosunga nyumba ya zobvala, Turutsira otumikira Baala onse zobvala. Nawaturutsira zobvala.
23. Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.