2 Atesalonika 3:15-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Koma musamuyese mdani, kama mumuyambirire ngati mbale.

16. Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.

17. Cilankhulo ndi dzanja langa Paulo; ndico cizindikilo m'kalata ali yense; ndiko kulemba kwanga.

18. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.

2 Atesalonika 3