9. ndiye amene kudza kwace kuli monga mwa macitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikilo ndi zozizwa zonama;
10. ndi m'cinyengo conse ca cosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza cikondi ca coonadi sanacisandira, kuti akapulumutsidwe iwo.
11. Ndipo cifukwa cace Mulungu atumiza kwa iwo macitidwe a kusoceretsa, kuti akhulupirire bodza;
12. kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira coonadi, komatu anakondwera ndi cosalungama.