2 Akorinto 8:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo tikudziwitsani, abale, cisomo ca Mulungu copatsika mwa Mipingo ya ku Makedoniya,

2. kuti m'citsimikizo cacikuru ca cisautso, kucurukitsa kwa cimwemwe cao, ndi kusauka kwaokweni kweni zidacurukira ku colemera ca kuolowa mtima kwao.

3. Pakuti monga mwa mphamvu yao, ndicitapo umboni, inde koposa mphamvu yao,

4. anacita eni ace, natiumirfza ndi kutidandauliraza cisomoco, ndi za ciyanjano ca utumiki wa kwa oyera mtima;

5. ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa cifuniro ca Mulungu.

6. Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, comweconso atsirize kwa inu cisomo icinso.

7. Koma monga mucurukira m'zonse, m'cikhulupiriro, ndi m'mau, ndi m'cidziwitso, ndi m'khama lonse, ndi m'cikondi canu ca kwa ife, curukaninso m'cisomo ici.

2 Akorinto 8