4. Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tiri nako mwa Kristu:
5. si kuti tiri okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mocokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kucokera kwa Mulungu;
6. amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la cilembo, koma la mzimu; pakuti cilembo cipha, koma mzimu ucititsa moyo.
7. Komangati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolocedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israyeli sanathe kuyang'anitsa pankhope yace ya Mose, cifukwa ca ulemerero wa nkhope yace, umene unalikucotsedwa:
8. koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala m'ulemerero?
9. Pakuti ngati utumiki wa citsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa cilungamo ucurukira muulemerero kwambiri.
10. Pakutinso cimene cinacitidwa ca ulemerero sicinacitidwa ca ulemerero m'menemo, cifukwa ca ulemerero woposawo.
11. Pakuti ngati cimene cirikucotsedwa cinakhala m'ulemerero, makamaka kwambiri cotsalaco ciri m'ulemerero.
12. Pokhala naco tsono ciyembekezo cotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukuru,