2 Akorinto 10:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kocurukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye ku kumangirira, ndipo si ku kugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;

9. kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa akalatawo.

10. Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lace ngofoka, ndi mau ace ngacabe.

11. Wotereyo ayese ici kuti monga tiri ife ndi mau mwa akalata, pokhala palibe ife, tiri oterenso m'macitidwe pokhala tiri pomwepo.

12. Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzibvomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwookha, alibe nzeru.

2 Akorinto 10