13. Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa cilekelezero cimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.
14. Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikira kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Kristu:
15. osadzitamandira popitirira muyeso mwa macititso a ena; koma tiri naco ciyembekezo kuti pakukula cikhulupiriro canu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa cilekezero cathu kwa kucurukira,