6. iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi; ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi.
7. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi,
8. Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.