1 Yohane 3:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacita cimo, cifukwa mbeu yace ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kucimwa, popeza wabadwa kucokera mwa Mulungu.

10. M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosacita cilungamo siali wocokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wace.

11. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira paciyambi, kuti tikondane wina ndi mnzace:

12. osati monga Kaini anali wocokera mwa woipayo, namupha mbale wace. Ndipo anamupha iye cifukwa ninji? Popeza nchiro zace zinali zoipa, ndi za mbaie wace zolungama.

13. Musazizwe, abale, Jikadana nanu dziko lapansi.

14. Ife tidziwa kuti tacokera kuturuka muimfa kulowa m'moyo, cifukwa tikondana ndi abale iye amene sakonda akhala muimfa.

15. Yense wakudana ndi mbale wace ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kun wakupha munthu ali yense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.

16. Umo tizindikira cikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wace cifukwa ca ife; ndipo ife tiyener kupereka moyo wathu cifukwa ca abale.

1 Yohane 3