19. Anaturuka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero 1 kuti aonekere kutr sali onse a ife.
20. Ndipo 2 inu muti nako kudzoza kocokera kwa Woyerayo, ndipo 3 mudziwa zonse.
21. Sindinakulemberam cifukwa simudziwa coonadi, koma cifukwa muddziwa, ndi cifukwa kulibe bodza locokera kwa coonadi.
22. 4 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Kristu? iye ndiye wokana Kristu, amene akana Atate ndi Mwana.
23. 5 Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wobvomereza Mwana ali ndi Atatenso.