13. Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kucenjeza, kulangiza.
14. Usanyalapse mphatsoyo iri mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa cinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.
15. Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.
16. Udzipenyerere wekha, ndi ciphunzitsoco. Uzikhala muizi; pakuti pocita ici udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.