1. Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya cikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosoceretsa ndi maphunziro a ziwanda,
2. m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olocedwa m'cikumbu mtima mwao monga ndi citsulo camoto;
3. akuletsa ukwati, osivitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti acikhulupiriro ndi ozindikira coonadi azilandire ndi ciyamiko.
4. Pakuti colengedwa conse ca Mulungu ncabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi ciyamiko;