1 Samueli 9:25-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumudzi, iye anakamba ndi Sauli pamwamba pa nyumba yace.

26. Ndipo anauka mamawa; ndipo kutaca, Samueli anaitana Sauli ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Sauli anauka, naturuka onse awiri, iye ndi Samueli, kunka kunja.

27. Ndipo pamene analikutsika polekeza mudzi, Samueli ananena ndi Sauli, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.

1 Samueli 9