1 Samueli 30:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ace ku Zikilaga tsiku lacitatu, Aamaleki adaponya nkhondo yobvumbulukira kumwera, ndi ku Zikilaga, nathyola Zikilaga nautentha ndi moto;

2. nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, akuru ndi ang'ono; sanapha mmodzi, koma anawatenga, namuka.

3. Ndipo pamene Davide ndi anthu ace anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao amuna ndi akazi anatengedwa ukapolo.

1 Samueli 30