1. Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisrayeli anamanga ku citsime ca m'Jezreeli.
2. Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ace ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi.
3. Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa acitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Sauli, mfumu ya Israyeli, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.