1 Samueli 28:4-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Sauli anasonkhanitsa Aisrayeli onse, namanga iwo ku Giliboa.

5. Ndipo pamene Sauli anaona khamu la Afilisti, anaopa, ndi mtima wace unanjenjemera kwakukuru.

6. Ndipo pamene Sauli anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankha ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.

1 Samueli 28