1 Samueli 28:22-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Cifukwa cace tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka.

23. Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ace, pamodzi ndi mkaziyo anamkangamiza; iyenamvera mau ao. Comweco anauka pansi, nakhala pakama.

24. Ndipo mkaziyo anali ndi mwana wa ng'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda cotupitsa;

25. nabwera nazo kwa Sauli ndi kwa anyamata ace; nadya iwowa. Atatero ananyamuka, nacoka usiku womwewo.

1 Samueli 28