3. Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ace, munthu yense ndi a pabanja pace, inde Davide ndi akazi ace awiri, Ahinoamu wa ku Jezreeli, ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wa Nabala.
4. Ndipo anauza Sauli kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunanso.
5. Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumiraga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wacifumu pamodzi ndi inu?
6. Ndipo Akisi anampatsa Zikilaga tsiku lomweli; cifukwa cace Zikilaga ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.