1 Samueli 23:19-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Sauli ku Gibeya, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango, m'phiri la Hakila. Umene Uri kumwera kwa cipululu?

20. Cifukwa cace mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m'mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m'dzanja la mfumu.

21. Sauli nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; cifukwa munandicitira ine cifundo.

22. Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m'mene akhalitsa, ndi amene adamuona m'menemo; cifukwa anandiuza kuti iye acita mocenjera ndithu.

23. Cifukwa cace yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.

24. Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Sauli; koma Davide ndi anthu ace anali ku cipululu ca Maoni, m'cigwa ca kumwera kwa cipululu.

25. Ndipo Sauli ndi anthu ace anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; cifukwa cace anatsikira kuthanthweko, nakhala m'cipululu ca Maoni. Ndipo pamene Sauli anamva ici, iye anamlondola Davide m'cipululu ca Maoni.

1 Samueli 23