1 Samueli 20:30-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Pamenepo Sauli anapsa mtima ndi Jonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Jeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?

31. Popeza nthawi yonse mwana wa Jeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Cifukwa cace tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu,

32. Ndipo Jonatani anayankha Sauli atate wace, nanena, Aphedwe cifukwa ninji? anacitanji?

33. Ndipo Sauli anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Jonatani anazindikira kuti atate wace anatsimikiza mtima kupha Davide.

34. Pamenepo Jonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku laciwiri la mwezi, pakuti mtima wace unali ndi cisoni cifukwa ca Davide, popeza atate wace anamcititsa manyazi.

1 Samueli 20