1 Samueli 17:41-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula cikopa cace anamtsogolera.

42. Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata cabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.

43. Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine garu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide nachula milungu yace.

44. Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za kuthengo.

1 Samueli 17