1 Samueli 15:32-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo Samueli anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleki. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.

33. Ndipo Samueli anati, Monga lupanga lako linacititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samueli anamdula Agagi nthuli nthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.

34. Pamenepo Samueli ananka ku Rama; ndi Sauli anakwera kunka ku nyumba yace ku Gibeya wa Sauli.

1 Samueli 15