1. Momwemo pakutaya coipa conse, ndi cmyengo conse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kadoka, ndi masiniiriro onse,
2. lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda cinyengo, kuti mukakule nao kufikira cipulumutso;
3. ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima;
4. amene pakudza kwa iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,
5. inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kun mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu,