6. M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukacitidwe cisoni ndi mayesero a mitundu mitundu,
7. kuti mayesedwe a cikhulupiriro canu, ndiwo a mtengo wace woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ocitira ciyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu, Kristu;
8. amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi, cimwemwe cosaneneka, ndi ca ulemerero:
9. ndi kulandira citsiriziro ca cikhulupiriro canu, ndico cipulumutso ca moyo wanu.