1. Ndipo Aisrayeli onse anawerengedwa mwa cibadwidwe cao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israyeli; ndipo Yuda anatengedwa ndende kumka ku Babulo cifukwa ca kulakwa kwao.
2. Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwao mwao m'roidzi mwao, ndiwo Israyeli, ansembe, Alevi, ndi Anetini.
3. Ndipo m'Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efraimu ndi Manase:
4. Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omri, mwana wa Imri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.
5. Ndipo a Asiloni: Asaya woyamba, ndi ana ace.
6. Ndi a ana a Zera: Yeueli ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.
7. Ndi a ana a Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodavia, mwana wa Hasenuwa;