1 Mbiri 7:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndi ana a Bekeri: Zemira, ndi Yoasi, ndi Eliezeri, ndi Eliunai, ndi Omri, ndi Yeremoti, ndi Abiya, ndi Anatoti, ndi Alemeti. Onsewa ndiwo ana a Bekeri.

9. Ndipo anayesedwa mwa cibadwidwe cao, mwa mibadwo yao, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi makumi awiri mphambu mazana awiri.

10. Ndi mwana wa Yedyaeli: Bilani; ndi ana a Bilani: Yeusi, ndi Benjamini, ndi Ehudi, ndi Kenana, ndi Zetani, ndi Tarasisi, ndi Ahisabara.

11. Onsewa ndiwo ana a Yedyaeli; ndiwo akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi khumi mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana awiri akuturuka kugulu kunkhondo.

12. Sufimu yemwe ndi Hupimu ana a Iri, ndi Husimu mwana wa Aheri.

13. Ana a Nafuali: Yazieli, ndi Guni, ndi Yezeri, ndi Salumu, ana a Bila.

14. Ana a Manase ndiwo Asrieli amene mkazi wace anambala, Koma mkazi wace wamng'ono Maramu anabala Makiri atate wa Gileadi;

15. ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wace wa Hupimu ndi Supimu, dzina lace ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana waciwiri wa Manase ndiye Tselofekadi. Ndi Tselofekadi anali ndi ana akazi.

1 Mbiri 7