1 Mbiri 5:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Beera mwana wace, amene Tigilati Pilesere wa ku Asuri anamtenga ndende; ndiye kalonga wa Arubeni.

7. Ndi abale ace monga mwa mabanja ao, powerenga cibadwidwe ca mibadwo yao: akuru ndiwo Yeyeli, ndi Zekariya,

8. ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoeli, wokhala ku Aroeri, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-meoni;

9. ndi kum'mawa anakhala mpaka polowera kucipululu kuyambira mtsinje wa Firate; pakuti zoweta zao zinacuruka m'dziko la Gileadi.

10. Ndipo masiku a Sauli anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, amene adagwa ndi dzanja lao; ndipo anakhala m'mahema mwao kum'mawa konse kwa Gileadi.

11. Ndi ana a Gadi anakhala pandunji pao m'dziko la Basana mpaka Saleka:

12. Yoeli mkuru wao, ndi Safamu waciwiri, ndi Yanai, ndi Safati m'Basana;

13. ndi abale ao a; nyumba za makolo ao: Mikaeli, ndi Mesulamu, ndi Seba, ndi Yorai, ndi Yakani, ndi Ziya, ndi Eberi; asanu ndi awiri.

1 Mbiri 5