1 Mbiri 4:22-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yoasi, ndi Sarafa wolamulira m'Moabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe.

23. Iwo ndiwo oumba mbiya, ndi okhala m'Netaimu, ndi m'Gedera; anakhala komweko ndi mfumu m'nchito yace.

24. Ana a Simeoni: Nemueli, ndi Yamini, Yaribi, Zera, Sauli,

25. Salumu mwana wace, Mibsamu mwana wace, Misma mwana wace.

26. Ndi ana a Misma: Hamueli mwana wace, Zakuri mwana wace, Simei mwana wace.

27. Ndipo Simei anali nao ana amuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana akazi asanu ndi mmodzi; koma abale ace analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinacurukitsa ngati ana a Yuda.

28. Ndipo anakhala ku Beereseba, ndi Molada, ndi Hazarasuala,

29. ndi ku Bila, ndi ku Ezemu, ndi ku Toladi,

1 Mbiri 4