1. Ana a Yuda: Perezi, Hezroni, ndi Karmi, ndi Huri, ndi Sobala.
2. Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati.
3. Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezreeli, ndi Isma, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi,
4. ndi Penueli atate wa Gedoro, ndi Ezeri atate wa Husa. Awa ndi ana a Huri woyamba wa Efrata atate wa Betelehemu.
5. Ndipo Asuri atate wa Tekowa anali nao akazi awiri: Hela, ndi Naara.
6. Ndi Naara anambalira Ahuzamu, ndi Heferi, ndi Temeni, ndi Hahastario Iwo ndiwo ana a Naara.