4. Woyang'anira cigawo ca mwezi waciwiri ndiye Dodai M-ahohi ndi cigawo cace; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'cigawo cace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
5. Kazembe wacitatu wa khamu wa mwezi wacitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkuru; ndi m'cigawo mwacemunalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.
6. Benaya ameneyo ndiye wamphamvu uja wa makumi atatu aja, woyang'anira makumi atatu aja; woyang'anira cigawo cace ndi Amizabadi mwana wace.
7. Wacinai wa mwezi wacinai ndiye Asebeli mbale wa Yoabu, ndi pambuyo pace Zebadiya mwana wace; ndi m'cigawo mwace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.