A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ace odziwa mphamvu cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang'anira Israyeli tsidya lino la Yordano kumadzulo, kuyang'anira nchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu.