5. awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m'mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yace. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana amuna khumi ndi anai, ndi ana akazi atatu.
6. Onsewa anawalangiza ndi atate wao ayimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
7. Ndipo ciwerengo cao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa ayimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.