5. Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.
6. Ndi Semaya mwana wa Netaneli mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleke mwana wa Abyatara, a akuru a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lace ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.
7. Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, waciwiri Yedaya,
8. wacitatu Harimu, wacinai Seorimu,
9. wacisanu Malikiya, wacisanu ndi cimodzi Miyamini,
10. wacisanu ndi ciwiri Hakozi, wacisanu ndi citatu Abiya,