1 Mbiri 21:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Satana anaukira Israyeli, nasonkhezera Davide awerenge Israyeli.

2. Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa akuru a anthu, Kawerengeni Israyeli kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe ciwerengo cao.

3. Nati Yoabu, Yehova aonjezere pa anthu ace monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? nanga afuniranji cinthuci mbuyanga, adzaparamulitsa Israyeli bwanji?

1 Mbiri 21