1. Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yace m'manja a Afilisti.
2. Anakanthanso Moabu; ndi Amoabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso,
3. Ndipo Davide anakantha Hadarezeri mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wace ku mtsinje wa Firate.