33. Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzapfuula mokondwera pamaso pa Yehova;Pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi,
34. Yamikani Yehova; pakuti iye ndiye wabwino;Pakuti cifundo cace ncosatha.
35. Nimunene, Tipulumutseni, Mulungu wa cipulumutso cathu;Mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu,Kuti tiyamike dzina lanu loyera,Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.
36. Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli,Kuyambira kosayamba kufikira kosatha.Ndipo anthu onse anati, Amen! nalemekeza Yehova.
37. Ndipo anasiyako ku likasa la cipangano la Yehova Asafu ndi abale ace, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;