1 Mbiri 16:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova.

3. Nagwira ali yense wa Israyeli, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi ncinci ya mphesa zouma.

4. Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israyeli.

5. Asafu ndiye mkuru wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Matitiya, ndi Eliabu, ndi Benaya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;

6. ndi Benaya ndi Yahazieli ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la cipangano la Mulungu.

7. Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ocita ndiwo Asafu ndi abale ace.

1 Mbiri 16